4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+