Yesaya 46:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Milungu imeneyi idzawerama, ndipo yonse pamodzi idzagwada pansi. Singapulumutse zifaniziro zawo+ zimene zanyamulidwa ngati katundu, koma idzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Yeremiya 43:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Nyumba za milungu ya Iguputo ndidzaziyatsa moto.+ Nebukadirezara adzatentha milunguyo ndi kuitenga kupita nayo kudziko lina. Monga mmene m’busa savutikira kuvala chovala chake,+ Nebukadirezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo ndi kuchokako atapambana.
2 Milungu imeneyi idzawerama, ndipo yonse pamodzi idzagwada pansi. Singapulumutse zifaniziro zawo+ zimene zanyamulidwa ngati katundu, koma idzatengedwa kupita ku ukapolo.+
12 Nyumba za milungu ya Iguputo ndidzaziyatsa moto.+ Nebukadirezara adzatentha milunguyo ndi kuitenga kupita nayo kudziko lina. Monga mmene m’busa savutikira kuvala chovala chake,+ Nebukadirezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo ndi kuchokako atapambana.