7 ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+ ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.+ Nsembe zawo zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zawo zina+ ndidzazilandira paguwa langa lansembe.+ Pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+