2 Ndinayamba kuona masomphenya ndipo ndinaona winawake wooneka ngati moto.+ Kuchokera pa chimene chinali kuoneka ngati chiuno chake kupita m’munsi, panali moto.+ Kuchokera m’chiuno mwake kupita m’mwamba, panali chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+