4 Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+