12 Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mu mdima?+ Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita m’chipinda chamkati mmene muli fano lake losema? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona.+ Yehova wachokamo m’dziko muno.’”