5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+
10 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira,+ ndipo uyenera kutumikira+ iye yekha basi.’”+