8 Ndiyeno mawu a mfumu ndi malamulo ake atamveka, komanso atsikana ambiri atawasonkhanitsa pamodzi kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani+ kuti Hegai+ aziwayang’anira, Esitere nayenso anam’tengera kunyumba ya mfumu komweko kuti Hegai woyang’anira akazi azimuyang’anira.