40 “Ndiyeno m’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwera+ idzayamba kukankhana nayo ndipo mfumu ya kumpoto idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi ndi zombo zambiri. Mfumuyo idzalowa m’mayiko ndi kudutsamo ngati madzi osefukira.