6 “Tsoka kwa anthu amene akukhala mwamtendere+ mu Ziyoni ndiponso anthu amene akumva kuti ndi otetezeka m’phiri la Samariya. Iwo ndiwo anthu olemekezeka a mtundu wotchuka pakati pa mitundu ina, ndipo nyumba yonse ya Isiraeli imabwera kwa anthu amenewa.