21 Kuyambira pamenepo, Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera kuti iye apite ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+
22 Kenako anati: “Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+