4 Tsopano Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo chikhamu cha anthu chinasonkhana kwa iye, mwakuti iye anakwera ngalawa n’kupita panyanjapo ndi kukhazikika chapatali pang’ono, koma khamu lonse la anthulo linakhala m’mphepete mwa nyanjayo.+