18 Koma kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Pa nthawi imene mayi ake Mariya anali atalonjezedwa+ ndi Yosefe kuti adzam’kwatira, Mariyayo anapezeka kuti ali ndi pakati mwa mzimu woyera+ asanatengane.
20 Koma ataganiza mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera m’maloto n’kumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba, chifukwa chakuti pakati alinapopa pachitika mwa mphamvu ya mzimu woyera.+