Mateyu 24:45 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 45 “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru+ amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+ Mateyu 25:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Mbuye wakeyo anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!+ Unakhulupirika+ pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti udziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’ Luka 19:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Iye anamuuza kuti, ‘Unagwira ntchito, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kukhulupirika pa chinthu chaching’ono, ndakupatsa ulamuliro woyang’anira mizinda 10.’+
45 “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru+ amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+
21 Mbuye wakeyo anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!+ Unakhulupirika+ pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti udziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’
17 Iye anamuuza kuti, ‘Unagwira ntchito, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kukhulupirika pa chinthu chaching’ono, ndakupatsa ulamuliro woyang’anira mizinda 10.’+