29 “Amuna inu, abale anga, ndilankhula ndithu mwaufulu za kholo lathu Davide. Iye anamwalira+ ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake tili nawo mpaka lero.
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro,+ ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo.+ Koma anawaona ali patali+ ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.+