14 Iye anayankha kuti: “Ndachitira nsanje kwambiri inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.”+