17 Ndiye chifukwa chake ndikukutumizirani Timoteyo,+ popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika+ mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu,+ monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.