33 Iye anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watitsanulira mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu.
55 Koma iye, pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.+
34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, zoonadi, amenetu anaukitsidwa kwa akufa. Iye ali kudzanja lamanja+ la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.+