12 Ndakulemberani m’mawu ochepa kudzera mwa Silivano,+ m’bale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi+ kuti ndikulimbikitseni ndi kupereka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu.+