Yesaya 13:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Nyama zam’tchire zokhala kumadera opanda madzi zidzagona kumeneko, ndipo nyumba za anthu amene anali kukhala kumeneko zidzadzaza ndi akadzidzi.+ Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko, ndipo ziwanda zooneka ngati mbuzi* zizidzadumphadumpha kumeneko.+ Yeremiya 50:39 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+ Yeremiya 51:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Babulo adzakhala milu yamiyala+ ndi malo obisalamo mimbulu.+ Adzakhala chinthu chodabwitsa ndi chochiimbira mluzu ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+
21 Nyama zam’tchire zokhala kumadera opanda madzi zidzagona kumeneko, ndipo nyumba za anthu amene anali kukhala kumeneko zidzadzaza ndi akadzidzi.+ Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko, ndipo ziwanda zooneka ngati mbuzi* zizidzadumphadumpha kumeneko.+
39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+
37 Babulo adzakhala milu yamiyala+ ndi malo obisalamo mimbulu.+ Adzakhala chinthu chodabwitsa ndi chochiimbira mluzu ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+