-
Genesis 41:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndiyeno Farao anagonanso nʼkulota maloto ena. Mʼmalotowa anaona ngala za tirigu 7 zikutuluka paphesi limodzi. Ngalazo zinali zokhwima ndi zazikulu bwino.+ 6 Pambuyo pake anaonanso ngala zina 7 zikutuluka. Ngalazo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa. 7 Ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zokhwima ndi zazikulu bwinozo. Kenako Farao anadzidzimuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.
-