35 Ana ake onse aamuna ndi aakazi ankapita kukamutonthoza, koma iye ankakana kutonthozedwa. Ankanena kuti: “Ayi! Ndidzalira mpaka kutsikira ku Manda*+ kumene kuli mwana wanga.” Ndipo bambo akewo anapitiriza kumulira.
20 Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, yemwe ndi wamngʼono kwa tonsefe.+ Mʼbale wake wa mimba imodzi anamwalira,+ moti anatsala yekha+ ndipo bambo amamukonda kwambiri.’