-
2 Petulo 2:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Koma anapulumutsa Loti yemwe anali munthu wolungama.+ Loti ankavutika kwambiri mumtima chifukwa cha khalidwe lopanda manyazi* limene anthu ophwanya malamulo ankachita. 8 (Munthu wolungamayu ankavutika mumtima tsiku ndi tsiku chifukwa cha zimene ankaona ndiponso kumva pamene ankakhala pakati pa anthu oipa. Iye ankavutika mumtima chifukwa cha zochita zawo zosamvera malamulo.) 9 Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova* amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.+ Koma anthu osalungama amawasunga kuti adzawawononge pa tsiku lopereka chiweruzo,+
-