-
Genesis 49:29-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Atatero anawalamula kuti: “Ine uno ndi ulendo wopita kumene kunapita makolo anga.*+ Mukandiike limodzi ndi makolo anga, mʼphanga limene lili mʼmunda wa Efuroni, Muhiti.+ 30 Ndithu mukandiike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure, mʼdziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda. 31 Kumeneko nʼkumene anaika Abulahamu ndi mkazi wake Sara.+ Nʼkumene anaika Isaki+ ndi mkazi wake Rabeka, ndipo nʼkumenenso ndinaika Leya. 32 Mundawo ndiponso phanga limene lili mmenemo, anagula kwa ana a Heti.”+
33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana akewo, anabwezeranso miyendo yake pabedi, nʼkumwalira. Kenako anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.*+
-
-
Genesis 50:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ana akewo anamunyamula nʼkupita naye kudziko la Kanani ndipo anakamuika mʼphanga mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda.+ 14 Yosefe ataika bambo ake mʼmanda, anabwerera ku Iguputo limodzi ndi abale ake ndi onse amene anamuperekeza pokaika bambo akewo.
-