-
Genesis 32:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tsiku limenelo Yakobo anagona pamalopo. Kenako anatenga zinthu zina pa chuma chake kuti akapatse mchimwene wake Esau ngati mphatso.+ 14 Anatenga mbuzi zazikazi 200, mbuzi zamphongo 20, nkhosa zazikazi 200, nkhosa zamphongo 20, 15 ngamila zoyamwitsa 30 ndi ana a ngamilazo, ngʼombe zazikazi 40, ngʼombe zamphongo 10, abulu aakazi 20 ndi abulu amphongo 10.+
-