-
Genesis 49:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Rubeni,+ iwe ndi mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka. Unayenera kukhala ndi ulemu waukulu ndi mphamvu zochuluka. 4 Koma sudzakhala wapamwamba kuposa abale ako, chifukwa mofanana ndi madzi osefukira unalephera kudziletsa, ndipo unakwera pogona pa bambo ako.+ Pa nthawiyo unadetsa* bedi langa. Anagonapo ndithu ameneyu!
-
-
1 Mbiri 5:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ana a Rubeni,+ mwana woyamba wa Isiraeli anali awa: Rubeni anali woyamba kubadwa koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo ake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo.
-