-
Ekisodo 31:2-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Inetu ndasankha* Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndidzamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse, 4 kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 5 waluso losema miyala ndi kupanga zoikamo miyala+ komanso wodziwa kupanga chilichonse chamatabwa.+
-