36 Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga* khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+
37 Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+