11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera chisa chake,
Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,
Mmene chimatambasulira mapiko ake, kuti chitenge anawo,
Nʼkuwanyamula pamapiko ake,+
12 Ndi Yehova yekha amene anapitiriza kumutsogolera,+
Panalibe mulungu wachilendo amene anali naye.+