3 Kwa zaka 6 muzikalima minda yanu, ndipo pa zaka 6 zimenezo muzidzadulira mitengo yanu ya mpesa ndi kukolola mbewu zanu.+ 4 Koma mʼchaka cha 7 dzikolo lizidzasunga sabata lopuma pa zonse, sabata la Yehova. Musamadzadzale mbewu mʼminda yanu kapena kudulira mitengo yanu ya mpesa.