-
Levitiko 24:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Utenge ufa wosalala nʼkuphika mikate 12 yozungulira yoboola pakati. Mkate uliwonse uzipangidwa ndi ufa wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* 6 Ndipo usanjikize mikateyo mʼmagulu awiri. Gulu lililonse likhale ndi mikate 6.+ Uike mikateyo patebulo lagolide woyenga bwino pamaso pa Yehova.+
-
-
2 Mbiri 13:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo akupereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼmawa uliwonse+ ndi madzulo alionse limodzi ndi mafuta onunkhira.+ Ndipo mikate yosanjikiza*+ ili patebulo la golide woyenga bwino. Komanso madzulo alionse+ amayatsa nyale zomwe zili pachoikapo nyale chagolide.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.
-