-
Ekisodo 36:8-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho anthu onse aluso+ anapanga chihema.+ Anachipanga ndi nsalu 10 zopangira tenti zopangidwa ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Iye* anapeta akerubi pa nsaluzo.+ 9 Nsalu iliyonse inali mamita 13* mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse muyezo wake unali wofanana. 10 Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi ndipo analumikizanso nsalu zina 5 zija pamodzi. 11 Atatero anapanga zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu imodzi pamene nsalu ziwirizo zidzalumikizane. Anachitanso chimodzimodzi mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, pamene nsaluzo zidzalumikizane. 12 Anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo kuti zikhale moyangʼanizana pamalo olumikizirana. 13 Pomaliza anapanga ngowe 50 zagolide nʼkulumikiza nsalu za tenti ndi ngowezo moti nsaluzo zinakhala chinsalu chimodzi chopangira chihema.
-