-
Ekisodo 36:14-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndiyeno anapanga nsalu za ubweya wa mbuzi zoyala pachihema. Anapanga nsalu 11.+ 15 Nsalu iliyonse inali mamita 13 mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse 11 muyezo wake unali wofanana. 16 Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi komanso analumikiza nsalu zina 6 pamodzi. 17 Atatero anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi. Anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo, pamalo amene nsalu ziwirizi zinalumikizana. 18 Atatero anapanga ngowe 50 zakopa zolumikizira nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi.
-