-
Ekisodo 36:20-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Kenako anapanga mafelemu oimika+ a chihema amatabwa a mthethe.+ 21 Felemu lililonse linali mamita 4 mulitali ndipo mulifupi linali masentimita 70. 22 Felemu lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri zoyandikana. Mafelemu onse a chihema anawapanga choncho. 23 Iwo anapanga mafelemu 20 a mbali yakumʼmwera ya chihemacho.
-