-
Ekisodo 36:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako anapanga zitsulo 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri anaziika pansi pa felemu lililonse ndipo munalowa zolumikizira ziwiri.+ 25 Kumbali ina ya chihemacho, mbali yakumpoto anaikako mafelemu 20, 26 ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse.
-