-
Ekisodo 36:27-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Anapanga mafelemu 6 nʼkuwaika kumbuyo kwa chihemacho, mbali yakumadzulo.+ 28 Anapanga mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza mʼmakona awiri akumbuyo kwa chihemacho. 29 Mafelemu amenewo anali ndi matabwa awiri ophatikiza kuyambira pansi mpaka pamwamba, pamene pali mphete yoyamba. Izi nʼzimene anachita ndi mafelemu onse ochirikiza mʼmakona. 30 Choncho anapanga mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse.
-