-
Ekisodo 36:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Ndiyeno anapanga ndodo zamtengo wa mthethe, ndodo 5 za mafelemu a mbali imodzi ya chihema,+ 32 ndi ndodo zinanso 5 za mafelemu a mbali ina ya chihema. Anapanganso ndodo zina 5 za mafelemu akumbuyo kwa chihema, mbali yakumadzulo. 33 Kenako anapanga ndodo yodutsa pakati pa mafelemu onse kuchokera koyambirira mpaka kumapeto.
-