-
Ekisodo 38:1-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa a mthethe. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, mulitali linali mamita awiri* ndipo mulifupi linalinso mamita awiri. Kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 134.+ 2 Anapanganso nyanga mʼmakona ake 4. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.* Atatero anakuta guwalo ndi kopa.*+ 3 Kenako anapanga ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. Anapanga ndowa, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko aakulu ndi zopalira moto. Ziwiya zake zonse anazipanga ndi kopa. 4 Guwalo analipangiranso sefa wa zitsulo zakopa. Analowetsa sefayo chapakati pa guwa lansembe, mʼmunsi mwa mkombero. 5 Analipangiranso mphete 4 mʼmakona ake 4 kuti muzilowa ndodo zonyamulira. Mphetezo anazilumikiza pafupi ndi sefa wa zitsulo zakopa. 6 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe, ndipo anazikuta ndi kopa. 7 Ndodozo anazilowetsa mumphetezo mʼmbali mwa guwa kuti zikhale zonyamulira guwalo. Guwa limenelo analipanga ngati bokosi lamatabwa losatseka pansi.
-