Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 38:9-15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndiyeno anapanga bwalo.+ Kumbali yakumʼmwera ya bwalolo anapangako mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake.+ 10 Panali zipilala 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 11 Kumbali yakumpoto, mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake. Zipilala zake 20 ndi zitsulo 20 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 12 Koma kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 23 mulitali mwake. Kunali zipilala 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 13 Mulifupi mwake kumbali yakumʼmawa, kotulukira dzuwa, mpandawo unali mamita 23. 14 Kumbali imodzi ya khomo la bwalo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 7. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo. 15 Ndipo kumbali ina ya khomo la bwalolo, mpandawo unali mamita 7 mulitali mwake. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena