-
Ekisodo 38:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Nsalu yotchinga pakhomo la bwalo anaiwomba ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Inali mamita 9 mulitali mwake, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba inali mamita awiri, mofanana ndi nsalu zotchingira mpanda wa bwalo.+ 19 Zipilala zake 4 ndi zitsulo 4 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilalazo tokolowekapo nsalu tinali tasiliva, ndipo pamwamba pa zipilalazo ndi tizitsulo tolumikizira anazikuta ndi siliva.
-