26 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala. Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wakumanja.