-
Ekisodo 30:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 “Kenako utenge mafuta onunkhira, abwino kwambiri awa: mule* woundana wokwana masekeli 500, sinamoni wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi wonunkhira wokwana masekeli 250. 24 Utengenso kasiya* masekeli 500 ofanana ndi masekeli akumalo oyera*+ komanso hini* imodzi ya mafuta a maolivi. 25 Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakanizidwa mwaluso.*+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.
-