Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 10:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ omwe ndi ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira, nʼkuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Atatero anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule.

  • 2 Mbiri 26:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iwo anapita pamene panali Mfumu Uziya kukamuletsa. Anamuuza kuti: “Mfumu Uziya, si zoyenera kuti inuyo mupereke nsembe zofukiza kwa Yehova.+ Ansembe okha ndi amene ayenera kupereka nsembe zofukiza chifukwa ndi mbadwa za Aroni+ ndipo anayeretsedwa. Tulukani mʼnyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika ndipo zimenezi sizikubweretserani ulemerero wochokera kwa Yehova Mulungu.”

  • Ezekieli 8:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndipo akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli anali ataimirira patsogolo pa mafanowo. Pakati pawo panalinso Yaazaniya mwana wa Safani.+ Aliyense ananyamula chiwaya chofukizira nsembe mʼmanja mwake ndipo utsi wonunkhira wa zofukizazo unkakwera mʼmwamba.+ 12 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mumdima? Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita mʼzipinda zake zamkati mmene muli mafano ake? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona. Yehova wachokamo mʼdziko muno.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena