-
Levitiko 5:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Koma ngati sangakwanitse kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ kuti ukhale nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lake. Asauthire mafuta ndipo asaikemo lubani chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo. 12 Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuimira nsembe yonseyo. Kenako auwotche paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yamachimo.
-