23 Ukamaliza kuyeretsa guwalo ku machimo, udzabweretse ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. 24 Udzazibweretse kwa Yehova ndipo ansembe adzaziwaze mchere+ nʼkuzipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu.