Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma ngati akupereka mbalame kuti ikhale nsembe yake yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, azipereka njiwa kapena ana a nkhunda.+

  • Levitiko 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa, azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ kuti zikhale nsembe zakupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+

  • Levitiko 14:21, 22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu. 22 Komanso azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, mogwirizana ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+

  • Luka 2:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Kumeneko iwo anapereka nsembe mogwirizana ndi zimene Chilamulo cha Yehova* chimanena kuti: “njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena