23 Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu chomwe si chopatulika. Ndipo aziwaphunzitsanso kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi chinthu choyera.+
7 Wansembe ayenera kuphunzitsa anthu za Mulungu. Anthu ayenera kupita kwa iye kuti akamve Chilamulo*+ chifukwa iye ndi mthenga wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.