38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa a mthethe. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, mulitali linali mamita awiri ndipo mulifupi linalinso mamita awiri. Kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 134.+