27 Kenako anawomba nsalu ya ulusi wabwino kwambiri nʼkupangira mikanjo ya Aroni ndi ana ake.+ 28 Anapanganso nduwira+ ya nsalu yabwino kwambiri, mipango yokongola yokulunga kumutu+ ya nsalu zabwino kwambiri ndi makabudula a nsalu+ za ulusi wopota wabwino kwambiri.