-
Levitiko 3:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Azipereka mbali ina ya nsembe yamgwirizanoyo ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ Azipereka mafuta+ okuta matumbo ndi mafuta onse amene ali pamatumbo. 4 Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo omwe ali pafupi ndi chiuno. Koma mafuta apachiwindi aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+ 5 Kenako ana a Aroni aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe, pamwamba pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni zimene zili pamoto.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+
-
-
Levitiko 7:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 “Uwauze Aisiraeli kuti, ‘Munthu amene akubweretsa nsembe yake yamgwirizano kwa Yehova,+ azipereka mbali ya nsembe yake yamgwirizanoyo kwa Yehova. 30 Iye azibweretsa yekha mafuta+ pamodzi ndi chidale ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. Ndipo aziyendetsa zinthu zimenezi uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku+ yoperekedwa kwa Yehova. 31 Wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe,+ koma chidalecho chizikhala cha Aroni ndi ana ake.+
-